Pakuti anadzitengera okha ndi ana amuna ao ana akazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.