Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiya m'ukapolo wathu, natifikitsira cifundo pamaso pa mafumu a Perisiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wace, ndi kutipatsa linga m'Yuda ndi m'Yerusalemu.