Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 31:6-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamacita mantha, kapena kuopsedwa cifukwa ca iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; iye sadzakusowani, kapena irukusiyani.

7. Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israyeli wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo.

8. Ndipo Yehova, iye ndiye amene akutsogolera; iye adzakhala ndi iwe, iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamacita mantha, usamatenga nkhawa.

9. Ndipo Mose analembera cilamulo ici, nacipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la cipangano la Yehova, ndi kwa akuru onse a Israyeli,

10. Ndipo Mose anawauza, ndi kuti, Pakutha pace pa zaka zisanu ndi ziwiri, pa nyengo yoikika ya m'caka cakulekerera, pa madyerero a misasa;

11. pakufika Israyeli wonse kuoneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene adzasankha, muzilalikira cilamulo ici pamaso pa Israyeli wonse, m'makutu mwao.

12. Sonkhanitsan; anthu, amuna ndi akazi ndi ana ang'ono, ndi mlendo wokhala m'midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kucita mau onse a cilamulo ici;

13. ndi kuti ana ao osadziwa amve, oaphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordano kulilandira likhale lanu lanu.

14. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'cihema cokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'cihema cokomanako.

15. Ndipo Yehova anaoneka m'cihema, m'mtambo njo; ndipo mtambo njo unaima pa khomo la cihema.

16. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, oadzatsata ndi cigololo milungu yacilendo ya dziko limene analowa pakati pace, nadzanditava Ine, ndi kutyola cipangano canga ndinapangana naoco.

17. Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zobvuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?

18. Koma Ine ndidzabisatu nkhope yanga tsiku lija cifukwa ca zoipa zonse adazicita; popeza anadzitembenukira milungu yina.

19. Ndipo tsopano mudzilemberere nyimbo iyi, ndi kuphunzitsa ana a Israyeli iyi: mulike m'kamwa mwao, kuti nyimbo iyi indicitire mboni yotsutsa ana a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 31