Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israyeli wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo.