Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 12:9-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. pakuti mpaka lero simunafikira mpumulo ndi colowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani.

10. Koma mudzaoloka Yordano, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.

11. Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.

12. Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu.

13. Dzicenjerani nokha, musamapereka nsembe zanu zopsereza pamalo ponse upaona:

14. koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mapfuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzicita zonse ndikuuzani.

15. Koma monga mwa cikhumbu conse ca moyo wanu muiphe ndi kudya nyama m'midzi yanu yonse, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani; odetsa ndi oyera adyeko, monga yamphoyo ndi yangondo.

16. Mwazi wao wokha musamadya; muziuthira panthaka ngati madzi.

17. Simukhoza kudya m'mudzi mwanu limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, kapena la vinyo wanu, kapena la mafuta anu, kapena oyambakubadwa a ng'ombe zanu kapena la nkhosa ndi mbuzi zanu, kapena zowinda zanu ziri zonse muzilonieza kapena nsembe zanu zaufulu, kapena nsembe yokweza ya m'dzanja lanu;

18. koma muzizidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'mudzi mwanu; nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'zonse mudazigwira ndi dzanja lanu.

19. Dzicenjerani nokha, musataye Mlevi masiku onse akukhala inu m'dziko mwanu.

20. Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu.

21. Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lace akakutanimphirani, muziphako ng'ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m'mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu.

22. Koma monga umo amadya mphoyo ndi ngondo momwemo uzizidya; odetsa ndi oyera adyeko cimodzimodzi.

23. Koma mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yace.

24. Musamadya uwu; muuthire pansi ngati madzi.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 12