Koma mudzaoloka Yordano, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.