Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 2:5-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Jabezi Gileadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munacitira cokoma ici mbuye wanu Sauli, ndi kumuika.

6. Ndipo tsopano Yehova acitire inu cokoma ndi coonadi; inenso ndidzakubwezerani cokoma ici, popeza munacita cinthuci.

7. Cifukwa cace tsono manja anu alimbike, nimucite camuna; pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.

8. Koma Abineri, mwana wa Neri, kazembe wa khamu la ankhondo a Sauli anatenga Isiboseti mwana wa Sauli, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;

9. namlonga ufumu wa pa Gileadi ndi Aasuri ndi Jezreeli ndi Efraimu ndi Benjamini ndi Aisrayeli onse.

10. Ndipo Isiboseti mwana wa Sauli anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israyeli, nacita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.

11. Ndipo Davide anali mfumu ya nyumba ya Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi.

12. Ndipo Abineri mwana wa Neri ndi anyamata a Isiboseti mwana wa Sauli anaturuka ku Mahanaimu kunka ku Gibeoni.

13. Ndi Yoabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anaturuka nakomana nao pa thamanda la Gibeoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo.

14. Ndipo Abineri ananena ndi Yoabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yoabu, Aimirire.

15. Pomwepo iwo anaimirira naoloka owerengedwa, khumi ndi awiri a kwa Benjamini, ndi Isiboseti mwana wa Sauli, ndi khumi ndi awiri a anyamata a Davide.

16. Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzace, nagwaza ndi lupanga lace m'nthiti mwa mnzaceo Comweco anagwa limodzi; cifukwa cace malo aja anachedwa Dera la Mipeni la ku Gibeoni.

17. Ndipo tsikulo nkhondo inakula ndithu. Ndi Abineri ndi anthu a Israyeli anathawa pamaso pa anyamata a Davide.

18. Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yoabu, Abisai ndi Asaheli. Ndipo Asaheli anali waliwiro ngati nyama ya kuthengo.

19. Ndipo Asaheli anapitikitsa Abineri. Ndipo m'kuthamanga kwace sanapambukira kulamanja, kapena kulamanzere, pakutsata Abineri.

20. Pomwepo Abineri anaceuka nati, Kodi ndi iwe Asaheli? iye nayankha, Ndine.

21. Ndipo Abineri ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zace. Koma Asaheli anakana kupambuka pakumtsata iye.

22. Ndipo Abineri anabwereza kunena kwa Asaheli, Pambuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yoabu?

23. Koma iye anakana kupambuka; cifukwa cace Abineri anamkantha ndi khali la mkondo m'mimba mwace, ndi khalilo linaturuka kumbuyo kwace. Ndipo anagwako, nafera pomwepo, Ndipo onse akufika kumalo kumene Asaheli anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 2