Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Jabezi Gileadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munacitira cokoma ici mbuye wanu Sauli, ndi kumuika.