Ndipo Isiboseti mwana wa Sauli anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israyeli, nacita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.