Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 14:28-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero cakudya. Ndipo anthuwo analema.

29. Ndipo Jonatani anati, Atate wanga wabvuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, cifukwa ndinalawako pang'ono uciwu.

30. Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? popeza tsopano palibe kuwapha kwakukuru kwa Afilisti.

31. Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ajaloni, ndipo anthu anafoka kwambiri.

32. Ndipo anthuwo anathamangira zowawanyazo, natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi ana a ng'ombe, naziphera pansi; anthu nazidya ziri ndi mwazi wao.

33. Pamenepo anauza Sauli, kuti, Onani anthu alikucimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munacita konyenga; kunkhunizani mwala waukuru kwa ine lero.

34. Ndipo Sauli anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yace, ndi munthu yense ndi nkhosa yace, aziphe pano, ndi kuzidya, osacimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yace, usiku uja naziphera pomwepo.

35. Ndipo Sauli anamangira Yehova guwa la nsembe; limenelo ndilo guwa loyamba iye anamangira Yehova.

36. Ndipo Sauli anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Citani ciri conse cikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Yehova kuno.

37. Ndipo Sauli anafunsira uphungu kwa Mulungu, Nditsikire kodi kwa Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja la Israyeli kodi? Koma iye sanamyankha tsiku lomweli.

38. Ndipo Sauli anati, Musendere kuno, inu nonse akuru a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m'mene muli coipa ici lero.

39. Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israyeli, cingakhale ciri m'mwana wanga Jonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.

40. Ndipo iye ananena ndi Aisrayeli onse, Inu mukhale mbali yina, ndipo me ndi Jonatani mwana wanga tidzakhala mbali yinanso. Ndipo anthuwo ananena ndi Sauli, Citani cimene cikukomerani.

41. Cifukwa cace Sauli ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israyeli, muonetse coonadi. Ndipo maere anagwera Sauli ndi Jonatani; koma anthuwo anapulumuka.

42. Ndipo Sauli anati, Mucite maere pakati pa ine ndi Jonatani mwana wanga. Ndipo anagwera Jonatani.

43. Pamenepo Sauli ananena ndi Jonatani, Undiuze cimene unacita. Ndipo Jonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uci pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 14