Pamenepo anauza Sauli, kuti, Onani anthu alikucimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munacita konyenga; kunkhunizani mwala waukuru kwa ine lero.