Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 14:17-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Pamenepo Sauli ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anaticokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Jonatani ndi wonyamula zida zace panalibe.

18. Ndipo Sauli ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israyeli.

19. Ndipo kunali m'mene Sauli anali cilankhulire ndi wansembeyo, phokoso la m'cigono ca Afilisti linacitikabe, nilikula; ndipo Sauli ananena ndi wansembeyo, Bweza dzanja lako.

20. Ndipo Sauli ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, naturukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzace ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukuru.

21. Ndiponso Ahebri akukhala nao Afilisti kale, amene anaturuka m'dziko lozungulira kukaiowa nao kuzithando; iwonso anatembenukira kuti akakhale ndi Aisrayeli amene anali ndi Sauli ndi Jonatani.

22. Anateronso Aisrayeli onse akubisala m'phiri la Efraimu, pakumva kuti Afilisti anathawa, iwo anawapitikitsa kolimba kunkhondoko.

23. Comweco Yehova anapulumutsa Israyeli tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni.

24. Ndipo Aisrayeli anasauka tsiku lija; pakuti Sauli anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere cilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya.

25. Ndipo anthu onsewo analowa munkhalango, panali uci pansi.

26. Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uci anacuruka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lace pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo.

27. Koma Jonatani sanamva m'mene atate wace analumbirira anthu; cifukwa cace iye ana tam balitsa ndodo ya m'dzanja lace, naitosa m'cisa ca uci, naika dzanja lace pakamwa pace; ndipo m'maso mwace munayera.

28. Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero cakudya. Ndipo anthuwo analema.

29. Ndipo Jonatani anati, Atate wanga wabvuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, cifukwa ndinalawako pang'ono uciwu.

30. Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? popeza tsopano palibe kuwapha kwakukuru kwa Afilisti.

31. Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ajaloni, ndipo anthu anafoka kwambiri.

32. Ndipo anthuwo anathamangira zowawanyazo, natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi ana a ng'ombe, naziphera pansi; anthu nazidya ziri ndi mwazi wao.

33. Pamenepo anauza Sauli, kuti, Onani anthu alikucimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munacita konyenga; kunkhunizani mwala waukuru kwa ine lero.

34. Ndipo Sauli anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yace, ndi munthu yense ndi nkhosa yace, aziphe pano, ndi kuzidya, osacimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yace, usiku uja naziphera pomwepo.

35. Ndipo Sauli anamangira Yehova guwa la nsembe; limenelo ndilo guwa loyamba iye anamangira Yehova.

36. Ndipo Sauli anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Citani ciri conse cikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Yehova kuno.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 14