Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 7:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma nyumba ya iye yekha Solomo anaimanga zaka khumi mphambu zitatu, natsiriza nyumba yace yonse.

2. Anamanganso nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano, m'litali mwace munali mikono zana limodzi, kupingasa kwace mikono makumi asanu, ndi msinkhu wace mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo.

3. Ndipo inayalidwa ndi mkungudza pamwamba pa zipinda makumi anai mphambu zisanu zolongosoledwa pa mapanda, mzere umodzi zipinda khumi mphambu asanu.

4. Ndipo panali mazenera m'mizere itatuyo, zenera limodzi lopenyana ndi linzace mizere itatu.

5. Ndipo makomo onse ndi mphuthu zonse zinali zamphwamphwa maonekedwe ace, ndipo zenera limodzi linapenyana ndi linzace mizere Itatu.

6. Ndipo anamanga khumbi la nsanamira, m'litali mwace munali mikono makumi asanu, kupingasa kwace mikono makumi atatu; ndipo panali khumbi lina patsogolo pace, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pacepo.

7. Ndipo anamanga khumbi la mpando wacifumu loweruziramo iye, ndilo khumbi la mirandu, ndipo linayalidwa ndi mkungudza pansi ndi posanja.

8. Ndipo nyumba yace yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khumbilo, linamangidwa cimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomo, yofanafana ndi khumbi limeneli.

9. Izi zonse zinali za miyala ya mtengo wapatali yosemasema, ya muyeso muyeso, yoceka ndi mipeni ya mano mana m'katimo ndi kunjako, kuyambira kumazikokufikira kumutu, momwemonso kunjako ku bwalo lalikuru,

10. Ndipo maziko ace anali a miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yaikulu, miyala ya mikono khumi, ndi miyala ya mikono isanu ndi itatu.

11. Ndi pamwamba pace panali miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yosemasema monga muyeso wace, ndi mitengo yamkungudza.

12. Ndipo bwalo lalikuru lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungundza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi likole la nyumbayo.

13. Ndipo mfumu Solomo anatuma anthu kukatenga Hiramu ku Turo.

14. Iyeyo anali mwana wace wa mkazi wamasiye wa pfuko la Nafitali, atate wace anali munthu wa ku Turo, mfundi wa mkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira nchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomo namgwirira nchito zace zonse.

15. Popeza iyeyu anaunda nsanamira ziwiri zamkuwa, msinkhu wace wa imodzi unali mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndipo cingwe ca mikono khumi mphambu iwiri cinayesa thupi la nsanamira imodzi.

16. Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kulika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wace wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzace mikono isanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 7