Ndipo nyumba yace yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khumbilo, linamangidwa cimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomo, yofanafana ndi khumbi limeneli.