Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 6:1-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunacitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto, caka cacinai cakukhala Solomo mfumu ya Israyeli, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi waciwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.

2. Ndipo nyumbayo mfumu Solomo anaimangira Yehova, m'litali mwace munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono makumi atatu.

3. Ndipo anamanga likole pakhomo pa nyumba ya kacisiyo, m'litali mwace munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwace mwa nyumbayo, kupingasa kwace kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.

4. Ndipo m'nvumbamo anamanga mazenera a made okhazikika.

5. Ndipo anamanga zipinda zosanjikizana zogundana ndi khoma, kuzungulira makoma a nyumba ya Kacisi, ndi monenera momwemo; namanga zipinda zozinga,

6. Cipinda capansico kupingasa kwace kunali mikono isanu, capakatico kupingasa kwace mikono isanu ndi umodzi, cacitatuco kupingasa kwace mikono isanu ndi iwiri; pakuti kubwalo anacepsa khoma pozungulirapo, mitanda isalongedwe m'makoma a nyumba.

7. Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveka: kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena cipangizo cacitsulo, pomangidwa iyo.

8. Khomo lolowera m'zipinda za pakati linali ku mbali ya ku dzanja lamanja ya nyumba; ndipo anthu amakwerera pa makwerero ozunguniza, kutikira ku zipinda za pakati, ndi kuturuka m'zapakatizo kulowa m'zacitatuzo,

9. Momwemo anamanga nyumbayo naitsiriza, naika mitanda, naifolera ndi matabwa amikungudza.

10. Ndipo anamanga zipindazo zogundana ndi nyumba yonseyo, cipinda ciri conse msinkhu wace mikono isanu; ndipo anazilumikizitsa kunyumba ndi mitengo yamkungudza.

11. Ndipo mau a Yehova anafika kwa Solomo, nati,

12. Kunena za nyumba yino ulikuimanga, ukamayenda iwe m'malemba anga, ndi kumacita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako.

13. Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israyeli osawasiya anthu anga a Israyeli.

14. Tsono Solomo anamanga nyumbayo naitsiriza.

15. Ndipo anacinga makoma a nyumba m'katimo ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi kufikira posanja, nacinga m'katimo ndi matabwa, nayala pansi m'nyumbamo matabwa amlombwa.

16. Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwace, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ici anamanga m'katimo cikhale monenera, malo opatulikitsa.

17. Ndipo nyumbayo, ndiyo Kacisi wa cakuno ca monenera, inali ya mikono makumi anai.

18. Ndipo m'kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gada; munali mikungudza yokha yokha simunaoneka mwala ai,

19. Ndipo anakonza monenera m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwace, kuikamo likasa la cipangano la Yehova.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 6