Kunena za nyumba yino ulikuimanga, ukamayenda iwe m'malemba anga, ndi kumacita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako.