Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Atsegula cosindikiza cacisanu ndi ciwiri. Angelo asanu ndi awiri, ndi malipenga oyamba anai

1. Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacisanu ndi ciwiri, munali cete m'Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.

2. Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.

3. Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala naco cotengera ca zofukiza cagolidi; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolidi, lokhala ku mpando wacifumu.

4. Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kuturuka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.

5. Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi mota wopara pa guwa la nsembe, nauponya pa dziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi cibvomezi.

6. Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe.

7. Ndipo woyamba anaomba, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosanganiza ndi mwazi, ndipo anazitaya pa dziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.

8. Ndipo mngelo waciwiri anaomba, ndipo monga ngati phiri lalikuru lakupserera ndi mota Iinaponyedwa m'nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi;

9. ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa ziri m'nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka.

10. Ndipo anaomba mngelo wacitatu, ndipo idagwa kucokera kumwamba nyenyezi yaikuru, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi;

11. ndipo dzina lace la nyenyeziyo alicha Cowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka cowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti anasanduka owawa.

12. Ndipo mngelo wacinai anaomba, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ace atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.

13. Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva ciombankhanga cirikuuluka pakati pa mwamba, ndi kunena ndi mau akuru, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padz'ko, cifukwa ca mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.