Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri

1. Ndipo ndinaona cizindikilo cina m'mwamba, cacikuru ndi cozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.

2. Ndipo ndinaona ngati nyanja yamandala yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene anaeilaka ciromboco, ndi fano lace ndi ciwerengero ca dzina lace, anaimirira pa nyanja ya mandala, nakhala nao azeze a Mulungu.

3. Ndipo ayimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Nchito zanu nzazikuru ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.

4. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Cifukwa Inu nokha muli woyera; cifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.

5. Ndipo zitatha izi ndinaona, ndipo panatseguka pa Kacisi wa cihema ca umboni m'Mwamba:

6. Ndipo anaturuka m'Kacisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atabvala mwala woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolidi pacifuwa pao,

7. Ndipo cimodzi ca zamoyo zinai cinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolidi zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.

8. Ndipo Kacisi anadzazidwa ndi utsi wocokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yace; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa m'Kacisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.