Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 8:21-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israyeli yense kuti olalirawo adagwira mudzi, ndi kuti utsi wa mudzi unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai.

22. A kumudzinso anawaturukira; potero anakhala pakati pa Israyeli, ena mbali yina, ena mbali yina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsala kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.

23. Koma mfumu ya ku Ai anamgwira wamoyo, nadza naye kwa Yoswa.

24. Ndipo kunali, atatha Israyeli kupha nzika zonse za ku Ai, kuthengo, kucipululu kumene anawapitikitsira, natha onse kugwa ndi lupanga lakuthwa mpaka adathedwa onse, Aisrayeli onse anabwerera ku Ai, naukantha ndi lupanga lakuthwa.

25. Ndipo onse amene adagwa tsiku lija, amuna ndi akazi, ndiwo zikwi khumi ndi ziwiri, anthu onse a ku Ai.

26. Popeza Yoswa sanabweza dzanja lace limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai.

27. Koma ng'ombe ndi zofunkha za mudzi uwu Israyeli anadzifunkhira monga mwa mau a Yehova amene analamulira Yoswa.

28. Ndipo Yoswa anatentha Ai, nausandutsa muunda ku nthawi yonse, bwinja kufikira lero lino.

29. Ndipo mfumu ya ku Ai, anampacika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wace pamtengo; ndipo anauponya polowera pa cipata ca mudzi; nauniikako mulu waukuru wamiyala, mpaka lero lino.

30. Pomwepo Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Israyeli guwa la nsembe m'phiri la Ebala,

31. monga Mose mtumiki wa Mulungu adalamulira ana a Israyeli, monga mulembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, guwa la nsembe la miyala yosasema, yoti palibe munthu anakwezapo citsulo; ndipo anafukizirapo Yehova nsembe zopsereza, naphera nsembe zoyamika.

32. Ndipo analembapo pa miyalayi citsanzo ca cilamulo ca Mose, cimene analembera pamaso pa ana a Israyeli.

33. Ndipo Aisrayeli onse, ndi akuru ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima cakuno ndi cauko ca likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenza likasa la cipangano la Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji pa phiri la Gerizimu, ndi ena pandunji pa phiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba pala kuti adalitse anthu a Israyeli,

34. Atatero, anawerenga mau onse a cilamulo, dalitso ndi temberero, monga mwa zonse zolembedwa m'buku la cilamulo.

35. Panalibe mau amodzi a zonse adazilamulira Mose osawerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Israyeli, ndi akazi ndi ang'ono, ndi alendo akuyenda pakati pao.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 8