Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 6:10-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo Yoswa analamulira anthu, ndi kuti, Musamapfuula, kapena kumveketsa mau anu, asaturuke konse mau m'kamwa mwanu, mpaka tsiku lakunena nanu ine, Pfuulani; pamenepo muzipfuula.

11. Ndipo anazungulitsa likasa la Yehova mudzi, kuzungulira kamodzi; pamenepo analowa kucigono, nagona m'mwemo.

12. Ndipo Yoswa analawira mamawa, ndi ansembe anasenza likasa la Yehova.

13. Ndipo ansembe asanu ndi awiri, akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo ndi kutsogolera nazo likasa la Yehova, anayenda ciyendere naliza mphalasazo; ndi okonzeka kunkhondowo anawatsogolera, ndi akudza m'mbuyo anatsata likasa la Yehova, ansembe ali ciombere poyenda iwo.

14. Ndipo tsiku laciwiri anazungulira mudzi kamodzi, nabwera kucigono; anatero masiku asanu ndi limodzi.

15. Ndipo kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri analawira mamawa, mbandakuca, nazungulira mudzi mommuja kasanu ndi kawiri; koma tsiku lijalo anazungulira mudzi kasanu ndi kawiri.

16. Ndipo kunali, pa nthawi yacisanu ndi ciwiri, pamene ansembe analiza mphalasa, Yoswa anati kwa anthu, Pfuulani; pakuti Yehova wakupatsani mudziwo.

17. Koma mudziwo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse ziri m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, cifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.

18. Ndipo inu, musakhudze coperekedwaco, mungadziononge konse, potapa coperekedwaco; ndi kuononga konse cigono ca Israyeli ndi kucisautsa.

19. Koma siliva yense, ndi golidi yense, ndi zotengera za mkuwa ndi citsulo zikhala copatulikira Yehova; zilowe m'mosungira cuma ca Yehova.

20. Ndipo anthu anapfuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anapfuula anthu ndi mpfuu yaikuru, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mudzi, yense kumaso kwace; nalanda mudziwo.

21. Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m'mudzi, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng'ombe, ndi nkhosa, ndi aburu, ndi lupanga lakuthwa.

22. Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m'nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kuturutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye.

23. Pamenepo anyamata ozondawo analowa, naturutsa Rahabi, ndi atate wace ndi mai wace ndi abale ace, ndi onse anali nao; anaturutsanso acibale ace onse; nawaika kunja kwa cigono ca Israyeli.

24. Ndipo anatentha mudzi ndi moto, ndi zonse zinali m'mwemo; koma siliva ndi golidi ndi zotengera zamkuwa ndi zacitsulo anaziika m'mosungira cuma ca nyumba ya Yehova.

25. Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wace, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israyeli mpaka lero tino; cifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko.

26. Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mudzi uwu wa Yeriko; adzamanga kuzika kwace ndi kutayapo mwana wace woyamba, nadzaimika zitseko zace ndi kutayapo mwana wace wotsirizira.

27. Potero Yehova anakhala ndi Yoswa; ndi mbiri yace inabuka m'dziko lonse.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 6