Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Malire a Yuda

1. Ndipo gawo la pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku cipululu ca Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.

2. Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mcere, ku nyondo yoloza kumwera;

3. naturuka kumwela kwa cikweza ca Akarabi, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Barinea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;

4. napitirira ku Azimoni, naturuka ku mtsinje wa Aigupto; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikuru; awa ndi malire anu a kumwera.

5. Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mcere, mpaka mathiriro ace a Yordano. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordano;

6. nakwera malire kumka ku Beti-hogila, napitirira kumpoto kwa Beti-araba; nakwera malire kumka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;

7. nakwera malire kumka ku Dibiri, kucokera ku cigwa ca Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa cikweza ca Adumi, ndiko kumwela kwa mtsinje; napitirira malire kumka ku madzi a Enisemesi, ndi maturukiro ace anali ku Eni-rogeli;

8. nakwera malire kumka ku cigwa ca mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwela, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kumka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ace a cigwa ca Refai kumpoto,

9. Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka citsime ca madzi ca Nefitoa, naturukira malire ku midzi ya phiri la Efroni; ndipo analemba malire kumka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.

10. Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kumka kumadzulo, ku phiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Beti-semesi, napitirira ku Timina;

11. naturuka malire kumka ku mbali ya Ekroni kumpoto; ndipo analemba malire kumka ku Sikeroni, napitirira ku phiri la Baala, naturuka ku Yabindi; ndipo maturukiro a malire anali kunyanja.

12. Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikuru ndiwo malire ace. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.

13. Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.

14. Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.

15. Nakwera komweko kumka kwa nzika za Dibiri; koma kale dzina la Dibiri ndilo Kiriyati-Seferi.

16. Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha Kiriyati-Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wace.

17. Ndipo Otiniyeli mwana wa Kenazi, mbale wace wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wace akhale mkazi wace.

18. Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wace kuti apemphe atate wace ampatse munda; ndipo anatsika pa buru; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?

19. Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwela, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.

20. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.

21. Ndipo midzi ya ku malekezero a pfuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwela ndiwo, Kabizeeli ndi Ederi, ndi Yaguri;

22. ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada;

23. ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi ltinani;

24. Zifi ndi Telemu ndi Bealoti;

25. ndi Hazorihadata, ndi Kerioti-hezirondi, ndiwo Hazori;

26. Amamu ndi Sema ndi Moloda;

27. ndi Hazara-gada, ndi Hesimoni, ndi Beti-peleti;

28. ndi Hazara-suala, ndi Beereseba, ndi Bizioti;

29. Baala, ndi lyimu, ndi Ezemu;

30. ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horima;

31. ndi Zikilaga, ndi Madimana ndi Sanasana;

32. ndi Lebaoti, ndi Siliimu, ndi Aini ndi Rimoni; midzi yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi miraga yao.

33. Ku cigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina;

34. ndi Zoona, ndi Eniganimu, Tapua, ndi Enamu;

35. Yarimutu, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka;

36. ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi miraga yao.

37. Zenani, ndi Hadasa, ndi Migidala-gadi;

38. ndi Dilani, ndi Mizipe, ndi Yokiteeli;

39. Lakisi ndi Bozikatu ndi Egiloni;

40. ndi Kaboni, ndi Lamasi, ndi, Kitilisi;

41. ndi Gaderotu, Beti-dagoni, ndi Naama, ndi Makeda; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.

42. Libina ndi Eteri ndi Asana;

43. ndi Ifita ndi Asina ndi Nezibi;

44. ndi Kehila ndi Akisibu, ndi Maresa; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi miraga yao.

45. Ekroni pamodzi ndi midzi yace ndi miraga yao;

46. kuyambira ku Ekroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodo, pamodzi ndi miraga yao.

47. Asidodo, midzi yace ndi miraga yace; Gaza, midzi yace ndi miraga yace; mpaka mtsinje wa Aigupto, ndi nyanja yaikuru ndi malire ace.

48. Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, om Soko;

49. ndi Dana, ndi Kiriyatisana, ndiwo Dibiri;

50. ndi Anabi, ndi Esitemo, ndi Animu;

51. ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; midzi khumi ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.

52. Arabu, ndi Duma, ndi Esana;

53. ndi Yanimu, ndi Beti-tapua, ndi Apeka;

54. ndi Humita, ndi Kiriyatiariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziori; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi miraga yao.

55. Maoni, Karimeli, ndi Zifu, ndi Yuta;

56. ndi Yesireeli, ndi Yokideamu, ndi Zoona;

57. Kaini, Gibea ndi Timina; midzi khumi pamodzi ndi miraga yao.

58. Haluli, Beti-zuru, ndi Gedori,

59. ndi Maaratu, ndi Bete-anotu, ndi Elitekoni; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.

60. Kiriyata-Baala, ndiwo KiriyatiYearimu ndi Raba; midzi iwiri pamodzi ndi miraga yao.

61. M'cipululu, Beti-araba, Midini, ndi Sekaka;

62. ndi Nibisani, ndi Mudzi wa Mcere, ndi En-gedi; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.

63. Koma ana a Yuda sanakhoza kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.