1. Ndipo maere aciwiri anamturukira Simeoni, pfuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi colowa cao cinali pakati pa colowa ca ana a Yuda.
2. Ndipo anali naco colowa cao Beeri-seba, kapena Seba, ndi Molada;
3. ndi Hazarasuala, ndi Bala, ndi Ezemu;
4. ndi Elitoladi, ndi Betuli, ndi Horimu;
5. ndi Zikilaga, ndi Beti-malikabotu, ndi Hazari-susa:
6. ndi Beti-lebaotu, ndi Saruheni; midzi khumi ndi itatu ndi miraga yao;
7. Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asana; midzi inai ndi miraga yao;
8. ndi miraga yonse yozungulira midzi iyi mpaka Baalata-beeri ndiwo Rama kumwera. Ndico colowa ca pfuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao.
9. M'gawo la ana a Yuda muli colowa ca ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawacurukira; cifukwa cace ana a Simeoni anali naco colowa pakati pa colowa coo.
10. Ndipo maere acitatu anakwecera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a colowa cao anafikira ku Saridi;
11. nakwera malire ao kumka kumadzulo ndi ku Marala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokineamu;
12. ndi kucokera ku Saridi anazungulira kumka kum'mawa kumaturukira dzuwa, mpaka malire a Kisilotu-tabori; naturuka kumka ku Daberati, nakwera ku Yafia;
13. ndi pocoka pamenepo anapitirira kumka kum'mawa ku Gati-heferi, ku Etikazini; naturuka ku Remoni umene ulembedwa mpaka ku Nea,
14. nauzungulira malire kumpoto, kumka ku Hanatoni; ndi maturukiro ace anali ku cigwa ca Ifita-eli;
15. ndi Kata, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi miraga yao.
16. Ici ndi colowa ca ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miraga yao.
17. Maere acinai anamturukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao.
18. Ndi malire ao anali ku Yezireeli, ndi Kesulotu, ndi Sunemu;
19. ndi Hafaraimu, ndi Sioni, ndi Anaharati;
20. ndi Rabiti ndi Kisioni, ndi Ebezi;
21. ndi Remeti ndi Eni-ganaimu ndi Eni-hada, ndi Beti-Pazezi;
22. ndi malire anafikira ku Tabori, ndi Sahazuma, ndi Betesemesi; ndi maturukiro a malire ao anali ku Yordano; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi ndi miraga yao.
23. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Isakara, monga mwa mabanja ao, midzi ndi miraga yao.
24. Ndipo maece acisanu analiturukira pfuko la ana a Aseri monga mwa mabanja ao.
25. Ndi malire ao ndiwo Helikati, ndi Hali, ndi Beteni ndi Akisafu;
26. ndi Alameleki, ndi Amadi, ndi Misali; nafikira ku Karimeli kumadzulo ndi ku Sihorilibinati;
27. nazungulira koturukira dzuwa ku Beti-dagoni, nafikira ku Zebuloni ndi ku cigwa ca Ifita-eli, kumpoto ku Beti-emeki, ndi Nehieli; naturukira ku Kabulu kulamanzere,
28. ndi Ebroni, ndi Rehobo, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkuru;
29. nazungulira malice kumka ku Rama, ndi ku mudzi wa linga la Turo; nazungulira malire kumka ku Hosa; ndi maturukiro ace anali kunyanja, kucokera ku Hebeli mpaka ku Akizibu;
30. Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobo; midzi makumi awiri mphambu iwiri ndi miraga yao,
31. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Aseri monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miragayao.
32. Maere acisanu ndi cimodzi anaturukira ana a Nafitali, ana a Nafitali monga mwa mabanja ao.
33. Ndipo malire ao anayambira ku Helefi, ku thundu wa ku Zaanani, ndi Adaminekebi, ndi Yabineeli, mpaka ku Lakumu; ndi maturukiro ace anali ku Yordano;
34. nazungulira malire kumka kumadzulo ku Azinotu-tabori, naturukira komweko kumka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Aseri kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordano kum'mawa.
35. Ndipo midzi yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti;
36. ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori;
37. ndi Kedesi, ndi Edrei, ndi Eni-hazori;
38. ndi Ironi, ndi Migidala-eli, Horemu, ndi Betianati, ndi Beti-semesi; midzi khumi ndi isanu ndi inai, ndi miraga yao.
39. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Nafitali, monga mwa mabanja ao, midzi ndi miraga yao.
40. Maere acisanu ndi ciwiri anaturukira pfuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao.
41. Ndipo malire a colowa cao anali Zora, ndi Esitaoli ndi Iri-semesi;
42. Saalabini, ndi Aijaloni ndi ltila;
43. ndi Eloni ndi Timna ndi Ekroni;
44. ndi Eliteke, ndi Gibetoni, ndi Baalati;
45. ndi Yehudi, ndi Bene-beraki, ndi Gatirimoni;
46. ndi Me-jarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pajapo.
47. Koma malire a ana a Dani anaturuka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, naucha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao.
48. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miraga yao.
49. Ndipo atatha kuligawa dziko likhale colowa cao monga mwa malire ace, ana a Israyeli anapatsa Yoswa mwana wa Nuni colowa pakati pao;
50. monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mudzi umene anawapempha, ndiwo Timinatisera, ku mapiri a Efraimu; ndipo anamangamudziwonakhala m'mwemo.
51. Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazare wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli, zikhale zao zao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la cihema cokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.