Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Midzi yopulumukirako

1. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

2. Nena ndi ana a Israyeli ndi kuti, Mudziikire midzi yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose,

3. kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalira inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.

4. Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa cipata ca mudziwo, nafotokozere mlandu wace m'makutu a akuru a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.

5. Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lace wakupha mnzaceyo; pakuti anakantha mnansi wace mosadziwa, osamuda kale.

6. Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wace, mpaka atafa mkulu wansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzace azibwerera ndi kufika kumudzi kwace, ndi nyumba yace, kumudzi kumene adathawako.

7. Ndipo anapatula Kedesi m'Galileya ku mapiri a Nafitali, ndi Sekemu ku mapiri a Efraimu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.

8. Ndipo tsidya lija la Yordano kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'cipululu, kucidikha, wa pfuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Gileadi wa ofuko la Gadi, ndi Golani m'Basana wa pfuko la Manase.

9. Iyi ndi midzi yoikidwira ana onse a Israyeli, ndi mlendo wakukhala pakati pao, kuti athawireko ali yense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.