Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 5:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Cifukwa cace mkango woturuka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene aturukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa ziri zambiri, ndi mabwerero ao acuruka.

7. Bwanji ndidzakhululukira iwe? pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anacita cigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama.

8. Anali onga akavalo okhuta mamawa; yense wakumemesera mkazi wa mnansi wace.

9. Kodi sindidzawalanga cifukwa ca zimenezi? ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera cilango mtundu woterewu?

10. Kwerani pa makoma ace nimupasule; koma musatsirize konse; cotsani nthambi zace pakuti siziri za Yehova.

11. Pakuti nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda zinandicitira monyenga kwambiri, ati Yehova.

12. Akana Yehova, ndi kuti, Si ndiye; coipa sicidzatifika ife; sitidzaona kapena lupanga kapena njala;

13. ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; comweco cidzacitidwa ndi iwo.

14. Cifukwa cace Yehova Mulungu wa makamu atero, Cifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.

15. Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutari, inu nyumba ya Israyeli, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene cinenero cace simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.

16. Phodo lao liri ngati manda apululu, onsewo ndiwo olimba.

17. Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako amuna ndi akazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga midzi yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.

18. Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 5