Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 31:4-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israyeli; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzaturukira masewero a iwo akukondwerera.

5. Ndiponso udzalima minda ya mphesa pa mapiri a Samariya; akunka adzanka, nadzayesa zipatso zace zosapatulidwa.

6. Pakuti lidzafika tsiku, limene alonda a pa mapiri a Efraimu adzapfuula, Ukani inu, tikwere ku Ziyoni kwa Yehova Mulungu wathu.

7. Pakuti Yehova atero, Yimbirirani Yakobo ndi kukondwa, pfuulirani mtundu woposawo; lalikirani, yamikirani, ndi kuti, Yehova, mupulumutse anthu anu, ndi otsala a Israyeli,

8. Taonani, ndidzatenga iwo ku dziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikuru lidzabwera kuno.

9. Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa ku mitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzapunthwa, pakuti ndiri Atate wace wa Israyeli, ndipo Efraimu ali mwana wanga woyamba.

10. Tamvani mau a Yehova, amitundu inu, lalikirani m'zisumbu zakutari; ndi kuti, Iye amene anabalalitsa Israyeli adzasonkhanitsa, nadzamsunga, monga mbusa acita ndi zoweta zace.

11. Pakuti Yehova wapulumutsa Yakobo, namuombola iye m'dzanja la iye amene anamposa mphamvu,

12. Ndipo adzadza nadzayimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira, ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikuru; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamicera; ndipo, sadzakhalanso konse ndi cisoni.

13. Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye cisoni cao.

14. Ndipo ndikhutitsa moyo wa ansembe ndi mafuta, ndipo anthu anga adzakhuta ndi zokoma zanga, ati Yehova.

15. Atero Yehova: Mau amveka m'Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakeli alinkulirira ana ace; akana kutonthozedwa mtima pa ana ace, cifukwa palibe iwo.

16. Yehova atero: Letsa mau ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti nchito yako idzalandira mphoto, ati Yehova; ndipo adzabweranso kucokera ku dziko la mdani.

17. Ndipo ciripo ciyembekezero ca citsirizo cako, ati Yehova; ndipo ana ako adzafikanso ku malire ao.

18. Kumva ndamva Efraimu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwana wa ng'ombe wosazolowera gori; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.

19. Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ncafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, cifukwa ndinasenza citonzo ca ubwana wanga.

20. Kodi Efraimu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; cifukwa cace mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamcitiradi cifundo, ati Yehova.

21. Taimitsa zizindikiro, udzipangire zosonyeza; taika mtima wako kuyang'anira mseu wounda, njira imene unapitamo; tatembenukanso, iwe namwali wa Israyeli, tatembenukiranso ku midzi yako iyi.

22. Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati; iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? pakuti Yehova walenga catsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.

23. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'midzi yace, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo cilungamo, iwe phiri lopatulika.

24. Ndipo Yuda ndi midzi yace yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 31