Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 29:19-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. cifukwa sanamvera mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova.

20. Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndacotsa m'Yerusalemu kunka ku Babulo.

21. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, za Ahabu mwana wace wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wace wa Maseya, amene anenera zonama m'dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo; ndipo Iye adzawapha pamaso panu;

22. ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali m'Babulo adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akucitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babulo inaoca m'moto;

23. cifukwa anacita zopusa m'Israyeli, nacita cigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.

24. Ndipo za Semaya Mnehelamu uzinena, kuti,

25. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, kuti, Cifukwa watumiza akalata m'dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wace wa Maseya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti.

26. Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'gori.

27. Ndipo tsopano, walekeranji kumdzudzula Yeremiya wa ku Anatoti, amene amadziyesa mneneri wanu,

28. popeza watitumizira mau ku Babulo, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zao?

29. Ndipo Zefaniya wansembe anawerenga kalata amene m'makutu a Yeremiya mneneri.

30. Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, akuti,

31. Uwatumizire mau am'nsinga onse, akuti, Atero Yehova za Semaya Mnehelamu: Cifukwa Semaya wanenera kwa inu, koma Ine sindinamtuma, ndipo anakukhulupiritsani zonama;

32. cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zace; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona za bwino ndidzacitira anthu anga, ati Yehova: cifukwa wanena zopikisana ndi Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 29