Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 9:24-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale lao lao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti acite nao cifuniro cao.

25. Ndipo analanda midzi yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zao zao nyumba zodza la ndi zokoma ziri zonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda yaazitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukuru.

26. Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya cilamulo canu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwacitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nacita zopeputsa zazikuru.

27. Cifukwa cace munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anapfuula kwa Inu, ndipo munamva m'Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.

28. Koma atapumula, anabwereza kucita coipa pamaso panu; cifukwa cace munawasiya m'dzanja la adani ao amene anacita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kupfuula kwa Inu, munamva m'Mwamba ndi kuwapulumutsa kawiri kawiri, monga mwa cifundo canu;

29. ndipo munawacitira umboni, kuti muwabwezerenso ku cilamulo canu; koma anacita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anacimwira malamulo anu (amene munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.

30. Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwacitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvera; cifukwa cace munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko.

31. Ndipo mwa nsoni zanu zocuruka simunawatha, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa cisomo ndi cifundo.

32. Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkuru, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi cifundo, asacepe pamaso panu mabvuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akuru athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asuri, mpaka lero lino.

33. Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwacita zoona, koma ife tacita coipa;

34. ndi mafumu athu, akuru athu, ansembe athu, ndi makolo athu, sanasunga cilamulo canu, kapena kumvera malamulo anu, ndi mboni zanu, zimene munawacitira umboni nazo.

35. Popeza sanatumikira Inu m'ufumu wao, ndi m'ubwino wanu wocuruka umene mudawapatsa, ndi m'dziko lalikuru ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerera kuleka nchito zao zoipa.

36. Tapenyani, ife lero ndife akapolo, ndi dzikoli mudalipereka kwa makolo athu kudya zipatso zace ndi zokoma zace, taonani, ife ndife akapolo m'menemo.

37. Ndipo licurukitsira mafumu zipatso zace, ndiwo amene munawaika atiweruze, cifukwa ca zoipa zathu; acitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zaweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukuru.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 9