Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 1 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Hoseya akwatira mkazi woipa kufanizira zoipa za Israyeli

1. MAU a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli.

2. Ciyambi ca kunena kwa Yehova mwa Hoseya, Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wacigololo ndi ana acigololo; pakuti dziko latsata cigololo cokha cokha kuleka kutsata Yehova.

3. Ndipo anamuka natenga Gomeri mwana wamkazi wa Diblaimu; iye naima, nambalira mwana wamwamuna.

4. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umuche dzina lace Yezreeli; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera cilango mwazi wa Yezreeli pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israyeli.

5. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ndidzatyola uta wa Israyeli m'cigwa ca Yezreeli.

6. Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umuche dzina lace Wosacitidwacifundo; pakuti sindidzacitiranso cifundo nyumba ya Israyeli, kuti ndiwakhululukire konse.

7. Koma ndidzacitira cifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.

8. Ataleka tsono kuyamwitsa Wosacitidwa cifundo, anaima, nabala mwana wamwamuna.

9. Ndipo Yehova anati, Umuche dzina lace Si-anthuanga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.

Israyeli acitidwa cifundo

10. Angakhale anatero, kuwerenga kwace kwa ana a Israyeli kudzanga mcenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.

11. Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israyeli adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkuru mmodzi, nadzakwera kucoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezreeli ndi lalikuru.