Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umuche dzina lace Wosacitidwacifundo; pakuti sindidzacitiranso cifundo nyumba ya Israyeli, kuti ndiwakhululukire konse.