Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Akwatiranso mkazi woipa, kufaniziranso zocita ana a Israyeli

1. Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lace, koma wakucita cigololo monga Yehova akonda ana a Israyeli, angakhale atembenukira ku milungu yina, nakonda ncinci za mphesa zouma.

2. M'mwemo ndinadzigulira iye ndi ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndi homeri ndi nusu wa barele;

3. ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usacita cigololo, usakhala mkazi wa mwamuna ali yense; momwemo inenso nawe.

4. Pakuti ana Israyeli adzakhala masiku ambiri a opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda coimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;

5. atatero ana a Israyeli adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wace masiku otsiriza.