Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Mulungu adandaulira Israyeli alape, nalonjeza kuwakhululukira

1. Israyeli, bwerera kumka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako.

2. Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Cotsani mphulupulu zonse, nimulandire cokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati: ng'ombe.

3. Asuri sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitil dzanenanso kwa nchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza cifundo.

4. Ndidzaciritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamcokera.

5. Ndidzakhala kwa Israyeli ngati mame; adzacita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yace ngati Lebano.

6. Nthambi zace zidzatambalala, ndi kukoma kwace kudzanga kwa mtengo waazitona, ndi pfungo lace ngati Lebano.

7. Iwo okhala pansi pa mthunzi wace adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, cikumbukilo cace cidzanga vinyo wa Lebano.

8. Efraimu adzati, Ndiri ndi cianinso ndi mafano? Ndayankha, ndidzampenyerera; ndiri ngati mtengo wamlombwa wabiriwiri; zipatso zako zipezeka zocokera kwa Ine.

9. Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? waluntha, kuti adziwe izi? pakuti njira za Yehova ziri zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.