Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 47:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yosefe analowa nauza Farao nati, Atate wanga ndi abale anga, ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao, ndi zonse ali nazo, anacokera ku dziko la Kanani; ndipo, taonani, ali m'dziko la Goseni.

2. Ndipo mwa abale ace anatengako anthu asanu, nawaonetsa iwo kwa Farao.

3. Ndipo Farao anati kwa abale ace, Nchito yanu njotani? ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu.

4. Nati kwa Farao, Tafika kuti tikhale m'dzikomo; popeza palibe podyetsa zoweta za akapolo anu; pakuti njala yakula m'dziko la Kanani. Mulole tsopano akapolo anu akhale m'dziko la Goseni.

5. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Atate wako ndi abale ako afika kwa iwe;

6. dziko la Aigupto liri pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga.

7. Ndipo Yosefe analowa naye Yakobo atate wace, namuika iye pamaso pa Farao; ndipo Yakobo anamdalitsa Farao.

8. Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati?

9. Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo angam'masikua ulendowao.

10. Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, naturuka pamaso pa Farao.

11. Ndipo Yosefe anakhazika atate wace ndi abale ace, napatsa iwo pokhala m'dziko la Aigupto, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramese, monga analamulira Farao.

12. Ndipo Yosefe anacereza atate wace ndi abale ace, ndi mbumba yonse ya atate wace ndi cakudya monga mwa mabanja ao.

13. Ndipo munalibe cakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; cifukwa cace dziko la Aaigupto ndi dziko la Kanani unalefuka cifukwa ca njalayo.

14. Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Aigupto ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama ku nyumba ya Farao.

15. Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Aigupto ndi m'dziko la Kanani, Aaigupto onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife cakudya; tiferenji pamaso panu? zatsirizika ndalama.

16. Ndipo Yosefe anati, Mundipatse ng'ombe zanu: ndipo ndidzakupatsani inu mtengo wa ng'ombe zanu ngati ndalama zatsirizika.

17. Ndipo anadza nazo ng'ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo cakudya cosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu; ndipo anawadyetsa iwo ndi cakudya cosinthana ndi zoweta zao zonse caka cimeneco.

Werengani mutu wathunthu Genesis 47