Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 17:10-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako zapambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu.

11. Muzidula khungu lanu; ndipo cidzakhala cizindikiro ca pangano pakati pa Ine ndi inu.

12. A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana amuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.

13. Azidulidwatu amene abadwa m'nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m'thupi mwako pangano losatha.

14. Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lace munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wace; waphwanya pangano langa.

15. Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamcha dzina lace Sarai, koma dzina lace ndi Sara.

16. Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amace a mitundu, mafumu a anthu adzaturuka mwa iye.

17. Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwace, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?

18. Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Ha! Ismayeli akhale ndi moyo pamaso panu!

19. Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamucha dzina lace Isake; ndipo ndidzalimbikitsa nave pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zace za pambuyo pace.

20. Koma za Ismayeli, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamcurukitsa iye ndithu; adzabala akaronga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukuru.

21. Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isake, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe yino caka camawa.

22. Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kucokera kwa Abrahamu.

23. Ndipo Abrahamu anatenga Ismayeli mwana wace ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwace, ndi onse, amene anagulidwa ndi ndalama zace, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwace kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.

Werengani mutu wathunthu Genesis 17