Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 45:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pogawa dziko likhale calowa cao, mupereke copereka kwa Yehova, ndico gawo lopatulika la dziko; m'litali mwace likhale la mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwace zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ace onse pozungulira pace.

2. Kutengako malo opatulika akhale nayo mikono mazana asanu m'litali mwace, ndi mazana asanu kupingasa kwace, lamphwamphwa pozungulira pace; ndi pabwalo pace poyera pozungulira pace mikono makumi asanu.

3. Ndipo kuyambira poyesedwapo uyese zikwi makumi awiri mphambu zili sanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace; m'menemo ndimo mukhale malo opatulika, ndiwo opatulika, ndiwo opatulikitsa.

4. Ndilo gawo lopatulika la dziko, ndilo la ansembe atumiki a malo opatulika, amene ayandikira kutumikira Yehova; apo ndipo amange nyumba zao, likhale malo a pa okha a: kwa malo opatulika.

5. Ndipo zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace, ndilo gawo la Alevi, atumiki a kacisi; likhale lao lao la midzi yokhalamo.

6. Ndipo dziko lace la mudziwo mulipereke la zikwi zisanu kupingasa kwace, ndi zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, pa mbali ya cipereko copatulika, ndilo la nyumba yonse ya Israyeli.

7. Ndipo kalonga adzakhala nalo gawo lace mbali yina ndi mbali inzace ya cipereko copatulika, ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa cipereko copatulika, ndi kutsogolo kwa dziko la mudzi, mbali ya kumadzulo kumadzulo, ndi mbali ya kum'mawa kum'mawa; ndi m'litali mwace mudzalingana ndi limodzi la magawo, kuyambira ku malire a kumadzulo kufikira malire a kum'mawa.

8. M'dzikomo ili lidzakhala lace lace m'Israyeli; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israyeli monga mwa mapfuko ao.

9. Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israyeli inu, lekani kucita ciwawa, ndi kulanda za eni ace; mucite ciweruzo ndi cilungamo; lekani kupitikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova.

10. Muzikhala nayo miyeso yoona, ndi efa woona, ndi bati loona.

11. Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri.

12. Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo mane wanu.

13. Copereka mucipereke ndico limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa tirigu; muperekenso limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa barele;

14. ndi gawo lonenedwa la mafuta, la bati wa mafuta, ndilo limodzi la magawo khumi la bati, kulitapa pa kori; ndiwo mabati khumi, ndiwo homeri; pakuti mabati khumi ndiwo homeri;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 45