Ndipo dziko lace la mudziwo mulipereke la zikwi zisanu kupingasa kwace, ndi zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, pa mbali ya cipereko copatulika, ndilo la nyumba yonse ya Israyeli.