Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 10:7-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Nabukitsa iwo mau mwa Yuda ndi Yerusalemu kwa ana onse otengedwa ndende, kuti azisonkhana ku Yerusalemu;

8. ndi kuti ali yense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akuru, cuma cace conse cidzaonongeka konse, ndipo iye adzacotsedwa ku msonkhano wa iwo otengedwa ndende.

9. Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wacisanu ndi cinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera cifukwa ca mlandu uwu, ndi cifukwa ca mvulayi.

10. Pamenepo Ezara wansembe ananyamuka, nanena nao, Mwalakwa, mwadzitengera akazi acilendo, kuonjezera kuparamula kwa Israyeli.

11. Cifukwa cace tsono, ululani kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, nimucite comkondweretsa; mudzilekanitse ndi mitundu ya anthu a m'dzikomo, ndi kwa akazi acilendo.

12. Ndipo unayankha msonkhano wonse, ndi kunena ndi mau akuru, Monga mwa mau anu tiyenera kucita.

13. Koma anthu ndiwo ambiri, ndi nyengo yino nja mvula, tiribenso mphamvu yakuima pabwalo, ndi nchitoyi sindiyo ya tsiku limodzi kapena awiri; pakuti tacurukitsa kulakwa kwathu pa cinthu ici.

14. Ayang'anire ici tsono akalonga athu a msonkhano wonse, ndi onse a m'midzi mwathu amene anadzitengera akazi acilendo abwere pa nthawi zoikika, ndi pamodzi nao akuru a mudzi wao uli wonse, ndi oweruza ace, mpaka udzaticokera mkwiyo waukali wa Mulungu wathu cifukwa ca mlandu uwu.

15. Yonatani mwana wa Asaheli ndi Yazeya mwana wa Tikiva okha anatsutsana naco, ndi Mesulamu ndi Sabetai Mlevi anawathandiza.

16. Pamenepo anthu otengedwa ndende anacita cotero. Ndi Ezara wansembe, ndi anthu akuru a nyumba za makolo, monga mwa nyumba za makolo ao, iwo onse ochulidwa maina ao anasankhidwa, nakhala pansi tsiku loyamba la mwezi wakhumi kufunsa za mlanduwu.

17. Natsiriza nao amuna onse adadzitengera akazi acilendo tsiku loyamba la mwezi woyamba.

18. Ndipo anapeza mwa ana a ansembe odzitengera akazi acilendo, ndiwo a ana a Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ace Maseya, ndi Eliezere, ndi Yaribu, ndi Gedaliya.

Werengani mutu wathunthu Ezara 10