Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 16:9-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Mudziwerengere masabata asanu ndi awiri; muyambe kuwerenga masabata asanu ndi awiri poyambira kuceka tirigu waciriri.

10. Ndipo mucitire Yehova Mulungu wanu madyerero a masabata, ndiwo msonkho waufulu wa dzanja lanu, umene mupereke monga Yehova Mulungu wanu akudalitsani.

11. Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace.

12. Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'Aigupto; musamalire kucita malemba awa.

13. Mudzicitire madyerero a misasa masiku asanu ndi awiri, mutasunga za padwale ndi za mopondera mphesa;

14. nimukondwere m'madyerero mwanu, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye okhala m'mudzi mwanu.

15. Masiku asanu ndi awiri mucitire Yehova Mulungu wanu madyerero m'malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zipatso zanu zonse, ndi m'nchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo.

16. Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene iye adzasankha, katatu m'caka; pa madyerero a mkate wopanda cotupitsa, pa madyerero a masabata, ndi pa madyerero a misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;

17. apereke yense monga mwa mphatso ya m'dzanja lace, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani.

18. Mudziikire oweruza ndi akapitao m'inidzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mapfuko anu; ndipo aweruze anthu ndi ciweruzo colungama.

19. Musamapotoza ciweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira cokometsera mlandu; popeza cokometsera mlandu cidetsa maso a anzeru, niciipsa mau a olungama.

20. Cilungamo, cilungamo ndico muzicitsata, kuti mukhale ndi moyo ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

21. Musamadziokera mitengo iri yonse ikhale nkhalango pafupi pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, limene mwadzimangira.

22. Ndipo musamadziutsira coimiritsa ciri conse cimene Yehova Mulungu wanu adana naco.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 16