Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 19:26-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira buru kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndiri wopunduka.

27. Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Yehova; cifukwa cace citani cimene cikukomerani.

28. Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjeze kudandaulira kwa mfumu?

29. Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.

30. Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere ku nyumba yace.

31. Ndipo Barizilai, Mgileadi anatsika kucokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordano ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordano.

32. Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka cakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.

33. Ndipo mfumu inanena ndi Barizilai, Tiyeni muoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu.

34. Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kumka ku Yerusalemu?

35. Lero ndiri nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira cimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oyimba? Cifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu.

36. Mnyamata wanu angofuna kuoloka Yordano pamodzi ndi mfumu; ndipo afuniranji mfumu kundibwezerapo mphothoyotere?

37. Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mudzi wanga ku manda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Cimamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumcitire cimene cikukomerani.

38. Ndipo mfumu inayankha, Cimamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamcitira cimene cikukomereni; ndipo ciri conse mukadzapempha kwa ine ndidzakucitirani inu.

39. Ndipo anthu onse anaoloka Yordano, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo Inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwace.

40. Comweco mfumu inaoloka nifika ku Giligala, ndi Cimamu anaoloka naye, ndipo anthu onse a Yuda adaolotsa mfumu, ndiponso gawo lina la anthu a Israyeli.

41. Ndipo onani, Aisrayeli onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakucotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lace pa Yordano, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye?

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 19