Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka cakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.