Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Chimo loopsa la Davide

1. Ndipo kunali pofikanso caka, nyengo yakuturuka mafumu, Davide anatumiza Yoabu, pamodzi ndi anyamata ace, ndi Aisrayeli onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsaliraku Yerusalemu.

2. Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wace nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wocititsa kaso pomuyang'ana.

3. Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu mkazi wa Uriya Mhiti?

4. Ndipo bavide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adacoka mumsambo; ndipo anabwereranso ku nyumba yace.

5. Ndipo mkaziyo anaima, natumiza munthu nauza Davide, kuti, Ndiri ndi pakati.

6. Davide natumiza kwa Yoabu, nati, Unditumizire Uriya Mhiti. Ndipo Yoabu anatumiza Uriya kwa Davide.

7. Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yoabu ali bwanji? ndi anthu ali bwanji? ndi nkhondo iri bwanji?

8. Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire ku nyumba yako, nutsuke mapazi ako, Ndipo Uriya anacoka ku nyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu.

9. Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wace, osatsikira ku nyumba yace.

10. Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsildra ku nyumba yace, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwera kuulendo? cifukwa ninji sunatsikira ku nyumba yako?

11. Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israyeli, ndi Yuda, alikukhala m'misasa, ndi mbuye wanga Yoahu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi ku nyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzacita cinthuci.

12. Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pane leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke, Comweco Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m'mawa mwace.

13. Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pace; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anaturuka kukagona pa kama wace pamodzi ndi anyamata a mbuye wace; koma sanatsildra ku nyumba yace.

14. Ndipo m'mawa Davide analembera Yoabu kalata, wopita nave Uriya.

15. Ndi m'kalatamo analemba kuti, Mumuike Uriya pa msongwe wa nkhondo yolimba, ndipo mumlekerere kuti akanthidwe nafe.

16. Ndipo Yoabu atayang'anira mudziwo, anaika Uriye pomwe anadziwa kuti pali ngwazi.

17. Ndipo akumudziwo anaturuka, namenyana ndi Yoabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Mhiti anafanso.

18. Pamenepo Yoabu anatumiza munthu nauza Davide zonse za nkhondoyi;

19. nauza mthengawo kuti, Utatsiriza kuuza mfumu zonse za nkhondozo;

20. kudzali kuti ukapsa mtima wa mfumu nikati kwa iwe, Cifukwa ninji munayandikira pafupi potere pamudzi kukamenyana nao? Simunadziwa kodi kuti apalingawo adzaponya?

21. Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Jerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Mhiti, iyenso adafa,

22. Comweco mthengawo unamuka, nufika, nudziwitsa Davide zonse Yoabu anamtumiza.

23. Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatilaka naturukira kwa ife kumundako, koma tinawa gwera kufikira polowera kucipata,

24. Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Mhiti, iyenso anafa.

25. Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yoabu, Cisakuipire ici, lupanga limaononga ina ndi mnzace. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamudzipo, nuupasule; numlimbikitse motere.

26. Ndipo pamene mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wace adamwalira, iye analira maliro a mwamuna wace.

27. Ndipo pakuturuka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao ku nyumba yace; ndipo iyeyo anakhala mkazi wace nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi cinthu cimene Davide adacita.