Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israyeli, ndi Yuda, alikukhala m'misasa, ndi mbuye wanga Yoahu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi ku nyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzacita cinthuci.