Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wace nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wocititsa kaso pomuyang'ana.