Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Nyimbo yoyamikira ya Davide

1. Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ace onse, ndi m'dzanja la Sauli.

2. Ndipo anati:-Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi mpulumutsi wanga, wangadi;

3. Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira;Cikopa canga, ndi nyanga ya cipulumutso canga, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga;Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuciwawa.

4. Ndidzaitanakwa Yehovaamene ayenera timtamande;Comweco ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.

5. Pakuti mafunde a imfa anandizinga,Mitsinje ya zopanda pace inandiopsa ine.

6. Zingwe za kumanda zinandizingira;Misampha ya imfa inandifikira ine.

7. M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova,Inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga;Ndipo Iye anamva mau anga ali m'kacisi wace,Ndi kulira kwanga kunafika ku makutuace.

8. Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira.Maziko a dziko la kumwamba anasunthikaNagwedezeka, cifukwa iye anakwiya.

9. M'mphuno mwace munaturuka utsi,Ndi moto woturuka m'kamwa mwace unaononga;Makala anayaka nao.

10. Anaweramitsa miyambanso, natsika;Ndipo mdima wandiwe-yani unali pansi pa mapazi ace.

11. Ndipo iye anaberekeka pa Kerubi nauluka;Inde anaoneka pa mapiko a mphepo,

12. Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira iye,Kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yocindikira ya mlengalenga.

13. Ceza ca pamaso paceMakala a mota anayaka,

14. Yehova anagunda kumwamba;Ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ace.

15. Ndipo iye anatumiza mibvi, nawawaza;Mphezi, nawaopsa,

16. Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka,Maziko a dziko anaonekera poyera,Ndi mthonzo wa Yehova,Ndi mpumo wa mweya wa m'mphuno mwace.

17. Iye anatumiza kucokera kumwamba nanditenga;Iye ananditurutsa m'madzi akuru;

18. Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,Kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu,

19. Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;Koma Yehova anali mcirikizo wanga,

20. Iye ananditurutsanso ku malo akuru;Iye anandipulumutsa, cifukwa akondwera ndi ine.

21. Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga;Monga mwa kuvera kwa manja anga anandipatsa mphotho.

22. Pakuti ndinasunga njira za Yehova,Osapambukira koipa kusiya Mulungu wanga.

23. Pakuti maweruzo ace onse anali pamaso panga;Ndipo za malemba ace, sindinawapambukira.

24. Ndinakhalanso wangwiro kwa iye,Ndipo ndinadzisunga kusacita kuipa kwanga.

25. Cifukwa cace Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga;Monga mwa kuyera kwanga pamaso pace.

26. Ndi acifundo Inu mudzadzionetsa wacifundo,Ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro;

27. Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;Ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.

28. Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;Koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwacepetse.

29. Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;Ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.

30. Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;Ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.

31. Kunena za Mulungu, njira yace iri yangwiro;Mau a Yehova anayesedwa; iye ndiye cikopa kwa onse akukhulupirira iye.

32. Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?

33. Mulungu ndiye Gnga langa lamphamvu;Ndipo iye ayendetsa angwiro mu njira yace.

34. Iye asandutsa mapazi ace akunga mapazi a mbawala;Nandiika pa misanje yanga.

35. Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;Kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.

36. Ndiponso munandipatsa cikopa ca cipulumutso canu;Ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.

37. Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,Ndi mapazi anga sanaterereka.

38. Ndinapitikitsa adani anga, ndi kuwaononga;Ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha.

39. Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka,Inde anagwa pansi pa mapazi anga.

40. Pakuti Inu munandimanga m'cuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; Munandigonjetsera akundiukira.

41. Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,Kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.

42. Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;Ngakhale kwa Yehova, koma iye sanawayankha.

43. Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati pfumbi la padziko,Ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala.

44. Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;Munandisunga ndikhale mutu wa amitundu;Anthu amene sindinawadziwa adzanditsumikira ine.

45. Alendo adzandigonjera ine,Pakumva za ine, adzandimbera pomwepo.

46. Alendo adzafota,Nadzabwera ndi kunthunthumira oturuka mokwiririka mwao.

47. Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;Ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la cipulumutso canga;

48. Inde Mulungu wakundibwezera cilango ine,Ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.

49. Amene anditurutsa kwa adani anga;Inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira;Mundipulumutsa kwa munthu waciwawa.

50. Cifukwa cace ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu,Ndipo ndidzayimba zolemekeza dzina lanu.

51. Iye apatsa mfumu yace cipulumutso cacikuru;Naonetsera cifundo wodzozedwa wace,Kwa Davide ndi mbeu yace ku nthawi zonse.