Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 1 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Amuuza Davide za imfa ya Sauli

1. NDIPO kunali atamwalira Sauli, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleki, ndipo Davide atakhala ku Zikilaga masiku awiri;

2. pa tsiku lacitatu, onani, munthu anaturuka ku zithando za Sauli, ali ndi zobvala zace zong'ambika, ndi dothi pamutu pace; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.

3. Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israyeti.

4. Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Sauli ndi Jonatani mwana wace anafanso.

5. Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwang kuti Sauli ndi Jonatani mwana wace anafa?

6. Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda pa phiri la Giliboa, ndinaona, Sauli alikuyedzamira nthungo yace, ndi magareta ndi apakavalo anamyandikiza.

7. Ndipo iye pakuceukira m'mbuyo mwace anandiona, nanditana. Ndipo ndinayankha, Ndine.

8. Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine M-amaleki.

9. Ndipo anati kwa ine, Uime pa ine nundiphe, cifukwa kuwawa mtima kwandigwera ine, popeza ndikali moyobe.

10. M'mwemo ndinakhala pambali pace ndi kumtsiriza cifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wace, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pace, ndi cigwinjiri ca pa mkono wace, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.

11. Pomwepo Davide anagwira zobvala zace nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye.

12. Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, cifukwa ca Sauli ndi mwana wace Jonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israyeli, cifukwa adagwa ndi lupanga.

13. Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuzayo, Kwanu nkuti? Nayankha, Ine ndine mwana wa mlendo, M-amaleki.

14. Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaopa kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova?

15. Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe, Ndipo anamkantha, nafa iye.

16. Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; cifukwa pakamwa pako padacita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.

Davide alirira Sauli ndi Jonatani

17. Ndipo Davide analirira Sauli ndi Jonatani mwana wace ndi nyimbo iyi ya maliro;

18. nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m'buku la Jasari:-

19. Ulemerero wako, Israyeli, unaphedwa pa misanje yako.Ha! adagwa amphamvu

20. Usacinene ku Gati,Usacibukitse m'makwalala a Asikeloni,Kuti ana akazi a Afilisti angasekere,Kuti ana akazi a osadulidwawo angapfuule mokondwera.

21. Mapiri inu a Giliboa,Pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka.Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa,Cikopa ca Sauli, monga ca wosadzozedwa ndi mafuta.

22. Uta wa Jonatani sunabwerera,Ndipo lupanga la Sauli silinabwecera cabe,Pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.

23. Sauli ndi Jonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao,Ndipo m'imfa yao sanasiyana; Anali nalo liwiro loposa ciombankanga,Anali amphamvu koposa mikango.

24. Ana akazi inu a Israyeli, mulirire Sauli,Amene anakubvekani ndi zofira zokometsetsa,Amene anaika zokometsetsa zagolidi pa zobvala zanu.

25. Ha! amphamvuwo anagwa pakati pa nkhondo!Jonatani anaphedwa pamisanje pako.

26. Ndipsinjika mtima cifukwa ca iwe, mbale wanga Jonatani;Wandikomera kwambiri;Cikondi cako, ndinadabwa naco,Cinaposa cikondi ca anthu akazi.

27. Ha! amphamvuwo anagwa,Ndi zida za nkhondo zinaonengeka,