Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Sauli ndi ana ace atatu aphedwa ndi Afilisti pa Giliboa

1. Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisrayeli; Aisrayeli nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Giliboa.

2. Ndipo Afilisti anapitikitsa, osawaleka Sauli ndi ana ace; ndipo Afilisti anapha Jonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisua, ana a Sauli.

3. Ndipo nkhondoyo inamkulira Sauli kwambiri, oponya mibvi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukuru cifukwa ca oponya mibviyo.

4. Tsono Sauli ananena ndi wonyamula zida zace, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka, Koma woo nyamula zida zace anakana; cifukwa anaopa ndithu. Cifukwa cace Sauli anatenga lupanga lace naligwera.

5. Ndipo pakuona kuti Sauli anafa, wonyamula zida zace yemwe, anagwera lupanga lace, nafera limodzi ndi iye.

6. Comweco adamwalira pamodzi Sauli ndi ana ace atatu, ndi wonyamula zida zace, ndi anthu ace onse, tsiku lomwe lija.

7. Ndipo pamene Aisrayeli akukhala tsidya lina la cigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordano, anaona kuti Aisrayeli alikuthawa, ndi kuti Sauli ndi ana ace anafa, iwowa anasiya midzi yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo.

8. Ndipo kunali m'mawa mwace, pakubwera Afilisti kubvula akufawo, anapeza Sauli ndi ana ace atatu ali akufa m'phiri la Giliboa.

9. Ndipo anadula mutu wace, natenga zida zace, natumiza m'dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira ku nyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu.

10. Ndipo anaika zida zace m'nyumba ya Asitarote; napacika mtembo wace ku linga la ku Betisani.

11. Koma pamene a ku Jabezi Gileadi anamva zimene Afilisti anamcitira Sauli,

12. ngwazi zonse zinanyamuka ndi kucezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Sauli, ndi mitembo ya ana ace, pa linga la Betisani; nafika ku Jabezi Gileadi naitentha kumeneko.

13. Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo uli m'Jabezi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.