Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Sauli ndi Jonatani mwana wace anafanso.