Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 6:18-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu pa dziko lapansi? taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?

19. Cinkana citero, labadirani pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lace, Yehova Mulungu wanga, kumvera kupfuula ndi kupempha kwace, kumene kapolo wanu apempha pamaso panu;

20. kuti maso anu atsegukire nyumba iyi usana ndi usiku, malo amene munanenerako kuti mudzaikako dzina lanu, kuti mumvere pemphero limene kapolo wanu adzapempha kuloza konkuno.

21. Ndipo mverani mapembedzero a kapolo wanu ndi a anthu anu Israyeli, popemphera iwo kuloza konkuno; ndipo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, ndipo pakumva Inu, mukhululikire.

22. Munthu akacimwira mnansi wace, ndipo akamuikira lumbiro lakumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira ku guwa lanu la nsembe, m'nyumba yino;

23. pamenepo mumvere m'Mwamba, nimucite ndi kuweruzira akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera chimo lace, ndi kulungamitsa wolungamayo, kumbwezera monga mwa cilungamo cace.

24. Ndipo anthu anu Israyeli akawakantha mdani cifukwa ca kukucimwirani, nakabwerera iwowa ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedzera pamaso panu m'nyumba yino;

25. pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire chimo la anthu anu Israyeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.

26. Mukatsekeka m'mwamba, mopanda mvula, cifukwa ca kukucimwirani; akapemphera iwo kuloza kumalo kuno, ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kwa zoipa zao, pamene muwasautsa;

27. pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire chimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Israyeli, mutawalangiza njira, yokoma ayenera kuyendamo, nimutumizire mvula dziko lanu limene munapatsa anthu anu likhale colowa cao.

28. Mukakhala njala m'dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala cinsikwi, kapena cinoni, dzombe, kapena kapuce; akawamangira misasa adani ao, m'dziko la midzi yao; mukakhala mliri uli wonse, kapena nthenda iri yonse;

29. pemphero ndi pembedzero liri lonse likacitika ndi munthu ali yense, kapena ndi anthu anu onse Aisrayeli, akadziwa yense cinthenda cace, ndi cisoni cace, nakatambasulira manja ace kuloza ku nyumba iyi;

30. pamenepo mumvere m'Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera ali yense monga mwa njira zace zonse, monga mudziwa mtima wace; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu;

31. kuti aope Inu, kuyenda m'njira zanu masiku onse akukhala iwo m'dziko limene munapatsa makolo athu.

32. Ndiponso kunena za mlendo wosakhala wa anthu anu Israyeli, akafumira ku dziko lakutari cifukwa ca dzina lanu lalikuru, ndi dzanja lanu lamphamvu, ndi mkono wanu wotambasuka; akadza iwowa ndi kupemphera kuloza ku nyumba iyi;

33. pamenepo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, nimumcitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi adziwe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisrayeli; ndi kuti adziwe kuti nyumba iyi ndamangayi ichedwa ndi dzina lanu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 6