Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 29:22-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Momwemo anapha ng'ombezo, ndi ansembe analandira mwazi, nauwaza pa guwa la nsembe, napha nkhosa zamphongozo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe; anaphanso ana a nkhosawo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe.

23. Pamenepo anayandikiza nao atonde a nsembe yaucimo pamaso pa mfumu ndi msonkhano; ndipo iwo anawasanjika manja ao,

24. ndi ansembewo anawapha, nacita nsembe yaucimo ndi mwazi wao pa guwa la nsembe, kucita cotetezera Aisrayeli onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yaucimo zikhale za Aisrayeli onse.

25. Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ace.

26. Alevi tsono anaimirira ndi zoyimbira za Davide, ndi ansembe anakhala ndi malipenga.

27. Nanena Hezekiya kuti apereke nsembe yopsereza pa guwa la nsembe. Ndipo pakuyamba nsembe yopsereza, inayambanso nyimbo ya Yehova ndi malipenga, pamodzi ndi zoyimbira za Davideyo mfumu ya Israyeli.

28. Ndi msonkhano wonse unalambira, ndi oyimbira anayimba, ndi amalipenga anaomba; zonsezi mpaka adatsiriza nsembe yopsereza.

29. Ndipo atatsiriza kuperekaku, mfumu ndi onse opezeka pamodzi naye anawerama, nalambira.

30. Hezekiya mfumu ndi akalonga anauzanso Alevi ayimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anayimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.

31. Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika ku nyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.

32. Ndi kuwerenga kwace kwa nsembe zopsereza unabwera nazo msonkhanowo ndiko ng'ombe makumi asanu ndi awiri, nkhosa zamphongo zana limodzi, ndi ana a nkhosa mazana awiri; zonsezi nza nsembe yopsereza ya Yehova.

33. Ndi zinthu, zopatulika zinafikira ng'ombe mazana asanu ndi limodzi, ndi nkhosa zikwi zitatu.

34. Koma ansembe anaperewera, osakhoza kusenda nsembe zonse zopsereza; m'mwemo abale ao Alevi anawathandiza, mpaka idatha nchitoyi, mpaka ansembe adadzipatula; pakuti Alevi anaposa ansembe m'kuongoka mtima kwao kudzipatula.

35. Ndiponso zidacuruka nsembe zopsereza, pamodzi ndi mafuta a nsembe zamtendere, ndi nsembe zothira za nsembe yopsereza iri yonse. Momwemo utumiki wa nyumba ya Yehova unalongosoka.

36. Nakondwera Hezekiya ndi anthu onse pa ici Mulungu adakonzeratu; pakuti cinthuci cidacitika modzidzimutsa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 29