Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 29:10-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Tsono mumtima mwanga nditi ndicite cipangano ndi Yehova Mulungu wa Israyeli, kuti mkwiyo wace waukali utembenuke kuticokera.

11. Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pace, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ace ndi kufukiza zonunkhira.

12. Pamenepo ananyamuka Alevi, Mahati mwana wa Amasai ndi Yoeli mwana wa Azariya, a ana a Akohati; ndi a ana a Merari, Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehaleleli; ndi a Agerisoni, Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa;

13. ndi a ana a Elizafana, Simri ndi Yeueli; ndi a ana a Asafu, Zekariya ndi Mataniya;

14. ndi a ana a Hemani, Yehudi ndi Simei ndi a ana a Yedutuni, Semaya ndi Uziyeli,

15. Ndipo anamemeza abale ao, nadzipatula, nalowa monga adawauza mfumu mwa mau a Yehova, kuyeretsa nyumba ya Yehova.

16. Ndipo ansembe analowa m'kati mwace mwa nyumba ya Yehova kuiyeretsa, naturutsira ku bwalo la nyumba ya Yehova zoipsa zonse anazipeza m'Kacisi wa Yehova. Nazilandira Alevi, kuziturutsira kunja ku mtsinje wa Kedroni.

17. Anayamba tsono kuipatula tsiku loyamba la mwezi woyamba, nafikira ku likole la Yehova tsiku lacisanu ndi citatu la mwezi, naipatula nyumba ya Yehova m'masiku asanu ndi atatu; natsiriza tsiku lakhumi ndi cisanu ndi cimodzi.

18. Pamenepo analowa m'katimo kwa mfumu Hezekiya, nati, Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, ndi guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zace zonse, ndi gome la mkate woonekera, ndi zipangizo zace zonse.

19. Zipangizo zonse zomwe adazitaya mfumu Ahazi m'ufumu wace m'kulakwa kwace kuja, tazikonza, ndi kuzipatula; ndipo taonani, ziri ku guwa la nsembe la Yehova.

20. Pamenepo mfumu Hezekiya analawira mamawa, nasonkhanitsa akalonga a m'mudzi, nakwera kumka ku nyumba ya Yehova.

21. Ndipoanabweranazong'ombe zisanundi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri, ndi atonde asanu ndi awiri, zikhale nsembe yaucimo ya ufumu, ndi ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Ndipo anawauza ansembe ana a Aroni azipereke pa guwa la nsembe la Yehova.

22. Momwemo anapha ng'ombezo, ndi ansembe analandira mwazi, nauwaza pa guwa la nsembe, napha nkhosa zamphongozo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe; anaphanso ana a nkhosawo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe.

23. Pamenepo anayandikiza nao atonde a nsembe yaucimo pamaso pa mfumu ndi msonkhano; ndipo iwo anawasanjika manja ao,

24. ndi ansembewo anawapha, nacita nsembe yaucimo ndi mwazi wao pa guwa la nsembe, kucita cotetezera Aisrayeli onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yaucimo zikhale za Aisrayeli onse.

25. Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 29