Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 18:4-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israyeli, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.

5. Pamenepo mfumu ya Israyeli anamemeza aneneri amuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Gileadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu.

6. Koma Yehosafati anati, Kulibenso kuno mneneri wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?

7. Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Yimla. Nati Yehosafati, Isatero mfumu.

8. Pamenepo mfumu ya Israyeli inaitana mdindo, niti, Katenge msanga Mikaya mwana wa Yimla.

9. Mfumu ya Israyeli tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wacifumu wace, obvala zobvala zacifumu zao, nakhala pamalo poyera polowera pa cipata ca Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.

10. Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zacitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adatha psiti.

11. Ndi aneneri onse ananenera momwemo, ndi kuti, Kwerani ku Ramoti Gileadi, mudzapindulako; pakuti Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.

12. Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu cokoma ngati m'kamwa m'modzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene cokoma.

13. Nati Mikaya, Pali Yehova, conena Mulungu wanga ndidzanena comweci.

14. Pamene anafika kwa mfumu, mfumu inanena naye, Mikaya timuke ku Ramoti Gileadi kunkhondo kodi, kapena ndileke? Nati iye, Kwerani, mudzacita mwai; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lanu.

15. Ndipo mfumu inati naye, Ndikulumbiritse kangati kuti unene nane coonadi cokha cokha m'dzina la Yehova?

16. Nati iye, Ndinaona Aisrayeli onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; nati Yehova, Awa alibe mbuye wao, abwerere yense ku nyumba yace mumtendere.

17. Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Sindinakuuzani kuti sadzandinenera zabwino koma zoipa?

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 18